Cookies on Plantwise Knowledge Bank

Like most websites we use cookies. This is to ensure that we give you the best experience possible.

 

Continuing to use www.plantwise.org/KnowledgeBank means you agree to our use of cookies. If you would like to, you can learn more about the cookies we use.

Plantwise Knowledge Bank

Your search results

PEST MANAGEMENT DECISION GUIDE: GREEN AND YELLOW LIST

Nchenche za mu Nyemba

Ophiomyia phaseoli Mphutsi zoononga tsidnde la Nyemba mu Chizungu
Zambia
 • Mubzale kuyambirira kwa nyengo (masiku 3-5 mvula yoyamba itagwa). Nchenche zopezeka mu nyemba zimakhala zocepekera kuyambilira ndipo tikamalowa mkati kwenikweni mwa nyengo nazo zimafalikira.
 • Chefulirani ndi kuika mayani ouma a nthoci kapena udzu kuthandizira kuti mbeu iike bwino mizu zke ndi kukhala yociteteza ku mphutsi.
 • Musabzale nyemba (binzi) pafupi ndi khobwe, soya kabena mbeu zina za mgulu la nyemba zimene zitha kubweretsa nchenche.
 • Cotsani ndi kuonong zonse zokhalira za mbeu zimene zionetsa kuonongedwa ndi nchenche cifukwa mphutsi zimapezeka mutsinde la mitengo ya nyemba. Koma ngati palibe tudoyo topereka ciopsezo kwambiri ndi kubweretsa matenda, conde lekani zokhalirazo zikhale munthaka kupereka cakudya m'nthakamo ndi kucepetsa kuphwa kwa madzi.
 • Mupange mizere kuundira kuti mizu ya mbeu itetezedwe patapita masabata 2-3 zitamera kuti mizu ikule mwamsanga.
 • Samalirani ndi kusunga adani acilengedwe, odana ndi nchenche za mu nyemba, adani monga mabvu, posafafaza mankhawala ophera tudoyo.
 • Mayani: Muone patside pa mayani pamwamba kuona ngati pali kuoneka zacikasu zoononga mayani komanso ngati pali mathotho patapita masabata 2-3 mbeu zitamera.
 • Tsinde: Onani ngati kuli zotupa, kapena zina zonetsa ziboowo zodyeramo tudoyo. Muone ngati pali mphutsi (zoyera) / nchenche zofikapo msinkhu (zakuda) munsi momwe tsinde likomana ndi dothi. Mucitepo kanthu ngati mwaona ziboowo za mphutsi pakati pa mitengo 3-4 yaikulu / sikweya mita
 • Mtengo wonse: Muone ngati pali mbali za cikasu, kulephera kukula, kuuma mayani ya mitengo ing'onoing'ono pamene ifika kukhala ndi mayani 2 mpaka 3. Mucitepo kanthu mukaona kuti mbeu 3-5 zili kufa mu mzere uli wonse pa sikweya mita (m2).
 • Mutenge adyo (galiki) 10, 2 anyenzi youma, ndi 6 mphilipili zouma ndipo muduledule zonsezo ndi kusakaniza. Mukatero ikani pamodzi ndi kuphika m'madzi a muyeso wa 1-2 litazi, muphike kwa mphindi 10, mutatha musiye kwa tsiku limodzi. Muonjezeko 1ml ya sopo wa madzi mu botolo kapena cotengera. Sambulusani 250ml kusakaniza ndi madzi okwanira 10 litazi. Mufafaze m'madzulo mulimonse patapita tsiku limodzi kwa masiku 5 kufikira mmutatha.
 • Nthawi zonse mukamagwiritsa nchito mankhwala ophera tidoyo (tizilombo) kapena kuika ku mbeu, bvalani zobvala zina zocinjiriza ndipo tsatirani malamulo ndi ndondomeko zolembedwa pomwepo monga nthawi, mulingo wace, nthawi yothilirapo, mofafazira, zoletsedwa kucita. Musataire mankhwalawo mopita madzi, ndi m'gwero la madzi.
 • Bungwe la za umoyo la WHO: Ululu wa mankhwala opezeka mu Gulu II la mankhwala ophera tizilombo mwina sungathe kuloledwa mu ndondomeko zina za masikimu ya IPM
 • Nthawi zonse onetsetsani kuti mugwiritsa nchito mndandanda wamankhwala ophera tizilombo obvomerezedwa ndi ZEMA
 • Muthire cabe pang'ono ku mbeu zing'onozing'ono. Mugwiritse nchito mankhwala okhala ndi Diazinon - (Diazon30EC, ndi ena); Organophosphate amaononga tudoyo podyedwa komanso popuma.
 • WHO gulu II (mankhawala aululu woononga); Musanalowemo REI masiku 5, musanakolole PHI masiku 21. Atha kupha ciswe, akangaude, nzimu (njuci), nyongolosi, nsomba. Mufafaze kamodzi kokha mutsinde mwa mbeu.
 • Mufafaze kumayani kuteteza ku nchenche zofikapo msinkhu: mankhwala okhala ndi Azadirachtin - (Nimu, NimbecidineE, ndi zina zotere). Mankhwala othawitsa, osadyedwa, komanso olepheretsa kuti tudoyo tukhale ndi mazira.
 • A cigawo ca zaumoyo ca WHO sanaike m'gulu mankhwalawa, koma satha kubweretsa ngozi pamene mugwiritsa bwino nchito; PHI masiku 3, REI tsiku 1. Mufafaze kamodzi kokha pomwe maluwa asanatuluke. Atha kupha ciswe, nzimu (njuci) ndi tudoyo tothandizira pa nthawi ya maluwa.
AUTHOR(S): Nthenga Isaiah, Zambia Agriculture Research Institute, Zambia, phone no. +260977208818, email: nthenga@gmail.com

CREATED/UPDATED: May 2015
PRODUCED BY: Plantwise

©CAB International. Published under a CC-BY-SA 4.0 licence.